Pulojekiti ya Tonse Tipindule ipereka mphamvu kwa aMalawi pankhani zamigodi - Mining & Trade Review (May 2017)

201705 Malawi Mining Trade Review Thoko Mapemba Norwegian Church Aid

Pulojekiti ya Tonse Tipindule ipereka mphamvu kwa aMalawi pankhani zamigodi

Kwa nthawi yaitali, anthu osauka a kumidzi yozungulira malo omwe kukuchitika ntchito za migodi akhala asakupindula nawo pa ntchitozo. Izi zili choncho chifukwa anthuwo sazindikira ndondomeko zina zoyendetsera migodi, komanso udindo omwe makampaniwo ali nawo pa anthuwo.

Anthuwo, mwachitsanzo, sazindikira kuti ali ndi udindo woonetsetsa kuti makampani a migodi akuteteza chilengedwe ndiponso kupereka gawo lina la chuma kuntchito zothandiza kutukulira miyoyo ya anthu m’madera ozungulira migodiyo (corporate social responsibility).

Koma vutoli tsopano lasanduka mbiri yakale m’madera chifukwa chakubwera kwa polojekiti yotchedwa Tonse Tipindule.

Pulojekitiyi ikugwiridwa ndi mgwirizano wamabungwe osiyanasiyana motsogoleredwa ndi a Norwegian Church Aid (NCA), ndi chithandizo cha ndalama chochokera ku Tilitonse Fund.

Cholinga cha ntchitoyi ndi kuonetsetsa kuti pali mgwirizano pakati pa anthu ozungulilidwa ndi ntchito za migodi, makampani a migodi ndiponso nthambi za boma zokhudzidwa ndi za migodi.

Mkulu oyanganira ntchitoyi ku NCA, a Thokozani Mapemba, ati ndi ndondomekoyi anthu akutha kuzindikira udindo wawo ndipo apatsidwa mphamvu zokamba ndi nthambi za boma komanso makampani pamomwe angapindulire ndi ntchito zamigodi.

Maboma asanu ndi anayi (nine) ndi komwe kukuchitika ntchitoyi ndipo mabomawa ndi a Chitipa, Karonga ndi Mzimba kuchigawo cha kumpoto. Madera ena ndi ku Balaka, Mangochi, Mwanza, Phalombe Mulanje ndi Ntcheu.

Mabungwe ena omwe akugwira nawo ntchitoyi ndi Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP), Episcopal Conference of Malawi (ECM), Evangelical Association of Malawi (EAM), Church and Society ya Livingstonia Synod, osaiwala a Qadria Muslim Association of Malawi (QMAM).

Zochitikachitika zokhudza ntchitoyi ndi monga kukonza misonkhano pakati pa aphungu a nyumba ya malamulo ndi anthu a m’midzi yozungulira migodi. Iwo amakambirana zamomwe malamulo angakonzedwere kuti ntchito zamigodi zizipindulira anthu akumudziwo.

Mkulu woyendetsa ntchitoyi ku bungwe la CCJP, a  Success Sikwese, ati kudzera mmisonkhano yomwe bungweli limakonza, anthu akutha kumasuka popereka maganizo awo mmene akufunira kuti ntchito za migodi ziziyendera.

Pa misonkhanoyi aphungu nawonso akumaonetsa  chidwi chofuna kukonza malamulo kuti azikomera mbali zonse zokhudzidwa ndi ntchito za migodi,

adatero a Sikwese.

***

This piece was initially published in Malawi’s Mining & Trade Review Issue Number 49 (May 2017).

The full edition is available for download here. This monthly publication is edited by Marcel Chimwala.

Advertisements

Leave a Comment, Question or Suggestion

Fill in your details below or click an icon to log in:

WordPress.com Logo

You are commenting using your WordPress.com account. Log Out / Change )

Twitter picture

You are commenting using your Twitter account. Log Out / Change )

Facebook photo

You are commenting using your Facebook account. Log Out / Change )

Google+ photo

You are commenting using your Google+ account. Log Out / Change )

Connecting to %s