Mutharika alola makampani kuyamba kufufuza mafuta - Mining & Trade Review (May 2017)

201705 Malawi Mining Trade Review James Chatupa Cassius Chiwambo Oil.png

Mutharika alola makampani kuyamba kufufuza mafuta

Mtsogoleri wa dziko lino Arthur Peter Mutharika wati dziko lino ndi lokonzeka kuyamba ntchito yofufuza mafuta kuchokera pansi pa Nyanja ya Malawi ndi madera ena kuphatikizapo kunsi kwa mtsinje wa Shire.

Kupezeka kwa mafuta mmaiko ena amuAfririka monga Uganda ndi Mozambique kwapangitsa kuti makampani akunja omwe ali ndi ukadaulo ofufuza and kukumba zitsime zamafuta aonetse chidwi choyamba kafukufuku wa mafuta m’dziko lino.

A  Mutharika atsimikizira a Malawi kuti asade nkhawa ndi zomwe mabungwe ena omwe siaboma akukamba  kuti ntchitoyi idzasokoneza chilengedwe, kuphatikizapo kupha nsomba zomwe zimapezeka mnyanja ya Malawi.

Munthu aliyense asadandaule ntchitoyi ikayamba chifukwa akatswiri adzagwiritsa ntchito njira zamakono kuti mafuta asasefukire nkuononga chilengedwe mnyanjayi.

Pamene mayiko ena muno muAfirika akugwira ntchito yofufuza mafuta, ifenso aMalawi sitiyenera kubwelera  m’mbuyo koma kupita patsogolo,

adatero a Mutharika ku Mangochi komwe kunali mwambo wokumbukira kufunikira kwa madzi, (World Water Day).

Nkhaniyi yakondweretsa akuluakulu okhudzidwa ndi nkhani zamigodi. Iwo ati zomwe walankhula Mutharika zikupereka chikhulupiliro kwa a Malawi kuti mtsogoleriyu ali ndi masomphenya komanso chidwi chofuna kutukula chuma chadziko lino.

A James chatupa omwe ndi mkulu wa kampani yomwe ili ndi ukadaulo ofufuza mafuta, yotchedwa Craton Resources, anawuza mtolankhani wa Mining and Trade   Review kuti sizoona kuti dziko la Malawi litsalire mmbuyo pankhani zamigodi pamene maiko ena akupindula kuchokera ku ntchito zomwezo.

Iwo anati chofunika nkusankha njira yofufuza mafuta yomwe ingapereke zotsatira zenizeni ndiponso zomwe zingateteze miyoyo ya nsomba panyanja ya Malawi.

Bungwe lamakampani a migodi la Malawi Chamber of mines nalonso lati ndi lokondwa ndi mawu a mtsogoleri wadziko linoyu.

Mmodzi mwa akuluakulu woyendetsa bungweli a Grain Malunga ati ntchitoyi iyenera kudzagwiridwa pogwiritsa njira zotsika mtengo kuti makampani amafutawa asazawononge ndalama zambiri koma adzatulutse zotsatira zenizeni.

Boma linapereka  ziphaso zopanga kafukufukuyu kumakampani ammaiko osiyanasiyana. Madera omwe kafukufukuyu akuchitika anagawidwa mzigawo zisanu ndi mphambu imodzi.

Gawo loyamba (Block 1) limayambira ku Chitipa kumalizira ku Karonga, ndipo idaperekedwa ku kampani ya ku South Africa yotchedwa Sac Oil Holdings. Kumpoto komweko kulinso  magawo ena awiri (Block 2 and 3) omwe ali panyanja yaMalawi ndipo adaperekedwa ku kampani ya Hamra Oil.

Magawo ena adagawidwa motere (Block 4 and 5) omwe akupezeka m’maboma a Nkhotakota, Salima, Dedza, Machinga, Blantyre and Mulanje adaperekedwa ku kampani ya Rak Gas MB45.

Gawo lomaliza (Block 6) lili pansi pa  kampani ya Pacific Oil. Gawoli lili m’maboma a Chikwawa ndi Nsanje komwe ndi kunsi kwa chigwa cha mtsinje wa Shire.

Mabungwe ena omwe siaboma motsogoleredwa ndi bungwe laku Britain la Oxfam akhala akunena kuti dziko lino silingayambe ntchito yofufuza mafuta chifukwa lilibe ndondomeko ya malamulo okhudza ntchitoyi.

Koma mkulu woyanganira ntchito zamafuta mu unduna wa zamigodi, a Cassius Chiwambo watsutsa za nkhaniyi. Iye wati malamulo alipo kale okhudza magwiridwe a ntchitoyi.

Malamulo analipo kale makampani asanapatsidwe zitupa zogwilira ntchitoyi mchaka cha 2011

adatero a Chiwambo.

Koma iwo adavomereza kuti nkofunikirabe kukonzanso ena mwa malamulo ogwilira ntchito za migodi ndi mafuta kuti ntchitozi zikhale zamphindu lokwanira kwa aMalawi.

Mchaka cha 2014, atatenga boma, a Mutharika adaimitsa kaye kupereka zitupa kwa makampani ofufuza mafuta ponena kuti dziko lino silili paliwiro pankhani zoyenga mafuta.

Makampani khumi ndi omwe adaonetsa chidwi chofuna kugwira ntchito yofufuza mafuta mchaka cha 2011 pomwe boma lidayamba kulandira makalata opempha kuyambitsa ntchitozi.

***

This piece was initially published in Malawi’s Mining & Trade Review Issue Number 49 (May 2017).

The full edition is available for download here. This monthly publication is edited by Marcel Chimwala.

Advertisements

Leave a Comment, Question or Suggestion

Fill in your details below or click an icon to log in:

WordPress.com Logo

You are commenting using your WordPress.com account. Log Out /  Change )

Google+ photo

You are commenting using your Google+ account. Log Out /  Change )

Twitter picture

You are commenting using your Twitter account. Log Out /  Change )

Facebook photo

You are commenting using your Facebook account. Log Out /  Change )

Connecting to %s